MULUNGU ADAPANGA DZIKO LATHU NDI ZAMOYO ZONSE
"Pachiyambi Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi." Genesis 1:1
"Pakuti mwa lye, zinalengedwa zonse za m'mwamba, ndi za padziko." Akolose 1:16a
"Odalitsika inu a kwa Yehova, Wakulenga kumwamba ndi dziko lapansi. Kunena za kumwamba, kumwamba ndiko kwa Yehova; Koma dziko lapansi analipereka kwa ana a anthu." Masalmo 115:15, 16
MULUNGU ADATIPANGA IFE
Ndipo
anati Mulungu, "Tipange munthu m'chifanizo chathu, monga mwa
chikhalidwe chathu: alamulire [ulamuliro] pa nsomba za
m'nyanja....ndi pa dziko lonse lapansi." Genesis 1:26a
MUNTHU ANAKHALA WAMOYO
"Ndipo Yehova Mulungu anaumba munthu ndi dothi lapansi, nauzira mpweya wa moyo m'mphuno mwake; munthuyo nakhala wamoyo*." Genesis 2:7
"Yehova Mulungu ndipo anati, `Si kwabwino kuti munthu akhale yekha; ndidzampangira womthangatira iye.' Koma Yehova Mulungu anamgonetsa Adamu tulo tatikuru, ndipo anagona: ndipo anatengako nthiti yake imodzi, natsekapo ndi mnofu pamalo pake: ndipo nthitiyo anaichotsa Yehova Mulungu mwa Adamu anaipanga mkazi, ndipo ananka naye kwa Adamu." Genesis 2:18, 21, 22
ADAMU NDI HAVA SADAMVERE MULUNGU
Tisamvere
nkomwe zotiuza Mdierekezi.
Ndipo Yehova Mulungu anatenga munthuyo, namuika iye m'munda wa Edene kuti aulime nauyang'anire. Ndipo Yehova Mulungu anamuuza munthuyo, nati "Mitengo yonse ya m'munda udyeko; koma mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoipa usadye umenewo; chifukwa tsiku lomwe udzadya umenewo udzafa ndithu." Genesis 2:15-17
NJOKA, YOTCHEDWANSO SATANA KAPENANSO KUTI MDIEREKEZI, SIDAKHULUPIRIRE MPHAMVU NDI ULAMULIRO WA MULUNGU NDIPO IDANENA BODZA.
Njokayo ndipo inati kwa mkaziyo, "Kufa simudzafai." Ndipo pamene anaona mkaziyo kuti mtengo unali wabwino kudya, ndi kuti unali wokoma m'maso mtengo wolakalakika wakupatsa nzeru, anatenga zipatso zake, nadya, napatsanso mwamuna wake amene ali naye, nadya iyenso. Genesis 3:4, 6
NDIPO ADAMU NDI HAVA SADATHE KUKHALANSO M'MUNDA MUJA
"Yehova
Mulungu anamturutsa iye m'munda wa Edene, kuti alime nthaka m'mene
anamtenga iye....Nakhazika Makerubi cha kum'mawa kwake...ndi lupanga
lamoto lakuzungulira ponsepo, lakusunga njira ya ku mtengo wa moyo."
Genesis 3:23, 24
LIDALI TSIKU LOMVETSA CHISONI MTUNDU WA ANTHU ONSE, PAMENE ADAMU NDI HAVA ADACHIMWA
"Monga uchimo unalowa m'dziko lapansi mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse...." Aroma 5:12b
CHIKONZERO CHANZERU CHA MULUNGU CHOTIWOMBOLERA IFE KU UCHIMO CHIDALI KUTUMIZA MWANA WAKE M'MODZI YEKHAYO
"Ndipo
adzabala mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yesu; pakuti
lyeyo adzapulumutsa anthu ake ku machimo
ao." Mateyu 1:21
YESU KRISTU NSEMBE YATHU YANGWIRO
Yesu
ndi Mwanawankhosa wa Mulungu. "Onani Mwanawankhosa wa Mulungu amene
achotsa tchimo lake la dziko lapansi!" Yohane 1:29b
Palibe nsembe yina yiliyonse yomwe yingachotse tchimo.
"Popeza tinayesedwa olungama [tinayesedwa opanda tchimo] ndi mwazi wake, makamaka ndithu tidzapulumuka mkwiyo wa Mulungu mwa Iyeyo." Aroma 5:9
Mbava
iyi sidakhulupirire Yesu, choncho sidapulumutsidwe .
"Kuti pokhala ife chikhalire ochimwa [osamvera Mulungu], Kristu adatifera ife." Aroma 5:8b
ONSE AMENE AKHULUPIRIRA MWA MWANA WA MULUNGU
ALI NAWO MOYO
"Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nao moyo wosatha." Yohane 3:16
"ANAUKA!"
Koma
mngelo anayankha, nati kwa akaziwo, "Musaope inu; pakuti ndidziwa inu
mulikufuna Yesu, amene anapachikidwa. Iye mulibe muno iai; pakuti
anauka, monga ananena. Idzani muno mudzaone malo m'mene anagonamo
Ambuye." Mateyu 28:5, 6
YESU AKHOZA KUKUPULUMUTSANI INU NDIPO AKUKUPEMPHERERANI
"Koma Iye chifukwa kuti akhala Iye nthawi yosatha ...komweko akhoza kupulumutsa konse konse iwo akuyandikira [kwathunthu] kwa Mulungu mwa Iye, popeza ali nao moyo wake chikhalire wa kuwapembedzera [wakuwadyolera] iwo." Ahebri 7:24, 25
M'MENE MUNGAPEZERE NJIRA YANU YA KWA MULUNGU
1.
Bvomerani kuti ndinu wochimwa (kuti simunamumvere
Mulungu).
"Pakuti onse anachimwa, naperewera pa ulemerero wa Mulungu." Aroma 3:23
2. Bwerani kwa Mulungu kudzera mwa Yesu Kristu.
"Kuchokera komweko akhoza kupulumutsa konse konse iwo akuyandikira kwa Mulungu mwa Iye." Ahebri 7:25a
3. Lapani machimo anu.
(kulapa kutanthauza kumva chisoni kwambiri koleka nako kuchimwa.)
"Chifukwa chake lapani, bwererani kuti afafanizidwe machimo anu." Machitidwe 3:19a
"Siyana nacho choipa, nuchite chokoma." Masalmo 37:27a
6.
Khulupirirani Yesu Kristu.
"Ngati udzabvomereza m'kamwa mwako [kuti] Yesu ndiye Ambuye, ndi kukhulupirira mumtima mwako kuti Mulungu anamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka." Aroma 10:9
7. Landirani Yesu Kristu mu mtima ndi m'moyo mwanu.
Inu nokha ndi amene mungatsekule chitseko cha mtima wanu ndi kuitana Yesu kuti alowemo. Yesu anati, "Taona, ndaima pakhomo, ndigogoda; wina akamva mau anga nakatsegula pakhomo, ndidzalowa kwa iye, ndipo ndidzadya naye, ndi iye ndi Ine." Chibvumbulutso 3:20
M'MENE MUNGAPEMPHERERE
Ngati simunapempherepo ndipo mufuna thandizo kuti muzipemphera, mukhoza kutsata pemphero lili m'munsili monga ngati chitsanzo chanu:
Okondedwa Ambuye Yesu,
Ndikuthokozani pondifera pamtanda kundichotsera machimo anga. Ndili womva chisoni pa zolakwa zanga zonse zomwe ndachita. Ndikupemphani kuti chonde bwerani mumtima mwanga ndikukhalamo muyaya. Ndikukhulupirirani Inu tsopano lino kuti muyeretse mtima wanga. Ndikulandirani Inu kuti mukhale Ambuye ndi Mpulumutsi wangawanga.
M'dzina la Yesu, Amen.
MUKAKHALA NDI YESU MUMTIMA MWANU, MULI NAWO MOYO WOSATHA
"Mulungu anatipatsa ife moyo wosatha, ndipo moyo umene[wu] uli mwa Mwana wake. Iye wakukhala ndi Mwana ali nao moyo." 1 Yohane 5:11b, 12a
"Iye wakumva mau anga, ndi kukhulupirira Iye amene anandituma Ine,...wachokera kuimfa, nalowa m'moyo." Yohane 5:24b
M'MENE MUNGASUNGIRE BWINO BWINO UDINDO WA KUTSATIRA YESU
"Lemba liri lonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso [chomwe inu mukhulupirira], chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m'chilungamo." 2 Timoteo 3:16
YESU AFUNA KUTI INU MUCHITIRE UMBONI KWA ENA
(kunyumba, kusukulu, kutchalitchi, ndiponso pena paliponse)
Yesu anati, "Ndipo sanamlola, koma ananena naye, Muka kwanu kwa abale ako, nuwauze zinthu zazikuru anakuchitira Ambuye, ndi kuti anakuchitira chifundo." Marko 5:19
KUMWAMBA NDI MALO ENIENI
M'masomphenya
a Yohane mu Chibvumbulutso 21 iye adaona m'mwamba mwatsopano ndi
dziko lapansi latsopano. Ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa
pamaso pao; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro,
kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita. Ndipo Iye
wakukhala pa mpando wachifumu anati, "Taonani, ndichita zonse zikhale
zatsopano." Chibvumbulutso 21:4, 5a
"...Mzindawo ngwa golidi woyengeka, wofanana ndi mandala oyera. Maziko a linga la mzinda anakometsedwa ndi miyala ya mtengo, ya mitundu mitundu." Chibvumbulutso 21:18b, 19b
YESU ANAPITA KUKAKONZA MALO OKHALAMO ONSE
OKHULUPIRIRA MWA IYE
"Mtima wanu usabvutike; mukhulupirira Mulungu, khulupirirani Inenso. M'nyumba ya Atate anga alimo malo okhalamo ambiri. Ngati sikudali kutero, ndikadakuuzani inu; pakuti ndipita kukukonzerani inu malo. Ndipo ngati ndipita kukakonzera inu malo, ndidzabweranso, ndipo ndidzalandira inu kwa Ine ndekha; kuti kumene kuli Ineko, mukakhale inunso." Yohane 14:1-3
Aliyense adzaukitsidwa kwa akufa. "Ikudza nthawi, imene onse ali m'manda adzamva mau ake, nadzaturukira, amene adachita zabwino, kukuuka kwa moyo; koma amene adachita zoipa kukuuka kwa kuweruza [kuchionongeko]." Yohane 5:28b, 29
Akufa mwa Kristu ndiwo amene adzauke poyamba. "Pamenepo ife okhala ndi moyo, otsalafe, tidzakwatulidwa nao pamodzi m'mitambo, kukakomana ndi Ambuye mumlengalenga, ndipo potero tidzakhala ndi Ambuye nthawi zonse." 1 Atesalonika 4:17
"Dikirani, pempherani: pakuti simudziwa nthawi yake." Marko 13:33b
KODI YESU ADZABWERA MOTANI?
"Taonani
adza ndi mitambo; ndipo diso liri lonse lidzampenya lye."
Chibvumbulutso 1:7a
Chenjerani ndi akristu onama ndi aneneri onama.
"Munthu akanena kwa inu, Onani, Kristu ali kuno, kapena uko musambvomereze. Onani, ali m'zipinda; musabvomereze." Mateyu 24:23b, 26
YESU ALINKUBWERA POSACHEDWA
M'MITAMBO YA M'MWAMBA
"Mitundu yonse ya pa dziko lapansi iddzadziguguda pachifuwa...nidzapenya Mwana wa munthu alinkudza pa mitambo ya kumwamba, ndi ulemerero waukuru." Mateyu 24: 30b